Fajr 04:42 Dhuhr 11:38 Asr 14:55 Maghrib 17:24 Isha 18:42
Blantyre, Malawi · Tuesday, 7 July 2026
News June 25, 2026 By MAM Communications 22 views

Mkumano Wa Ma Sheikh Pa NkhaniZa Uchembele Wabwino

Mkumano Wa Ma Sheikh Pa NkhaniZa Uchembele Wabwino

Bungwe la Muslim Association of Malawi, lero pa 3 June 2026 lachititsa mkumano wa ma Sheikh komanso anthu ena okhunzidwa.

Bungwe la Muslim Association of Malawi, lero pa 3 June 2026 lachititsa mkumano wa ma Sheikh komanso anthu ena okhunzidwa. 

 

Cholinga cha mkumanowu kunali kukambirna nkhani zokhunza kulumikizana pakati pa makolo ndi ana pa nkhani ya uchimbere wabwino. Iyi ndi imodzi ya mikumano imene bungwe la Nowergian Church Aid komanso Danish Charch Aid  ikuchittsa ndi cholinga chofuna kutolera mbalume zochokera ku mipingo ya mmene makolo angamayankhulanirane ndi ana awo pa nkhani ya uchembere. Potsilinza pa mikumanoyi palembedwa buku lomwe lingakhale ndi ziphunzitso za zipembenzo zosiyanasiyana kumphatikizapo chisilamu. 

 

MAM ndi limodzi mwa mabungwe  azipembenzo amene akugwira ntchito yolimbikitsa za uchembere wabwino kwa achinyamata  ndipo bungweli likugwira ntchitoyi m' boma la ntchitsi ndi nthandinzo la za chuma lochokera ku  Bumgwe la KFW la  ku Germany mosogozedwa ndi PSI komanso NCA-DCA kuno ku malawi. 

 

Ena mwa ma sheikh amene anali pa mkumanowu ndi Sh. Muhamad Silka, Sh. Bakar Danken, Sh. Omar Nkachelenga, Sh. Muslim Abass Vinjenje, Sh Swaleh Chilundu ndi ena ambili.